23 chilichonse chimene sichingapse ndi moto,+ chidutse pamoto kuti chikhale choyera. Muchiyeretsenso ndi madzi.+ Koma chilichonse chimene chingapse ndi moto muchiyeretse ndi madzi.+
16 Mizinda yokhayi ya anthu awa a mitundu ina imene Yehova Mulungu wanu akukupatsani monga cholowa, ndi imene simuyenera kusiyamo chilichonse chopuma chili chamoyo,+
2 Ukachite kwa Ai ndi mfumu yake zimene unachita kwa Yeriko ndi mfumu yake.+ Koma katundu ndi ziweto za mumzindawo mukafunkhe zikakhale zanu.+ Usankhe amuna ena oti akabisale kumbuyo kwa mzindawo.”+