12 Yoswa analanda mizinda yonse ya mafumuwa, ndi kugwira mafumu onse a mizindayi n’kuwapha ndi lupanga.+ Anawawononga onsewo+ monga mmene analamulira Mose mtumiki wa Yehova.+
11 “‘Kenako munawoloka Yorodano+ n’kufika ku Yeriko.+ Nzika za ku Yeriko, Aamori, Aperezi, Akanani, Ahiti, Agirigasi, Ahivi, ndi Ayebusi anayamba kumenyana nanu, koma ine ndinawapereka m’manja mwanu.+