13 Ndiyeno mfumu ya ana a Amoni inauza amithenga a Yefita kuti: “N’chifukwa chakuti Aisiraeli analanda dziko langa atatuluka mu Iguputo.+ Analanda dzikoli kuyambira ku Arinoni+ mpaka ku Yaboki ndi kukafikanso ku Yorodano.+ Tsopano undibwezere dzikoli mwamtendere.”