19 Pamenepo mzimu wa Yehova unayamba kugwira ntchito pa iye.+ Choncho anapita ku Asikeloni+ kumene anakapha amuna 30, ndipo anatenga zovala zawo n’kuzipereka kwa amene anamasulira mwambi aja.+ Koma mkwiyo wake unapitiriza kuyaka, ndipo anapita kunyumba ya bambo ake.