14 Choncho iye anafika ku Lehi, ndipo Afilisiti atamuona anafuula mokondwera.+ Pamenepo, mzimu wa Yehova+ unayamba kugwira ntchito pa iye, ndipo zingwe zimene anam’manga nazo manja zija zinaduka ngati ulusi wowauka ndi moto,+ moti zinadukaduka ndi kugwa.