12 Ndiyeno Delila anatenga zingwe zatsopano ndi kum’manga nazo, n’kumuuza kuti: “Afilisiti aja abwera Samisoni!” Pa nthawiyi n’kuti anthu atam’bisalira m’chipinda cha mkaziyo.+ Pamenepo, Samisoni anadula pakati zingwe zimene anam’manga nazo manjazo, ngati kuti akudula ulusi.+