9 Pamenepa n’kuti anthu atabisalira Samisoni m’chipinda cha mkaziyo,+ ndipo mkaziyo anamuuza kuti: “Afilisiti+ aja abwera Samisoni!” Pamenepo Samisoni anadula zingwe zija pakati, monga mmene ulusi wopota wabwazi umadukira ukayandikira moto.+ Ndipo chinsinsi cha mphamvu zake sichinadziwike.+