17 Tsopano Yakobo ananyamuka ulendo wopita ku Sukoti.+ Kumeneko anamanga nyumba yake ndi makola a ziweto zake.+ N’chifukwa chake malowo anawatcha kuti Sukoti.*
5 Ndiyeno iye anapempha amuna a ku Sukoti+ kuti: “Chonde, patsaniko anthu amene akunditsatirawa+ mitanda yobulungira ya mkate chifukwa ndi otopa, pakuti ndikuthamangitsa Zeba+ ndi Zalimuna,+ mafumu a Midiyani.”