24 Chakhumi chimene ana a Isiraeli azipereka kwa Yehova monga chopereka, ndawapatsa Alevi monga cholowa chawo. N’chifukwa chake ndinawauza kuti, ‘Asalandire cholowa pakati pa ana a Isiraeli.’”+
62 Onse amene anawerengedwa pakati pa Alevi analipo 23,000. Amenewa anali amuna onse kuyambira amwezi umodzi kupita m’tsogolo.+ Iwowa sanawerengedwe limodzi ndi ana a Isiraeli,+ chifukwa sanafunikire kulandira cholowa pakati pa ana a Isiraeli.+