Yoswa
14 Limeneli ndilo dziko limene ana a Isiraeli anatenga monga cholowa chawo m’dziko la Kanani.+ Wansembe Eleazara, Yoswa mwana wa Nuni, ndi atsogoleri a mafuko a makolo a ana a Isiraeli, ndiwo anagawa dzikolo kuti likhale cholowa chawo.+ 2 Anagawira cholowacho mafuko 9 ndi hafu, mwa kuchita maere,+ monga mmene Yehova analamulira kudzera mwa Mose.+ 3 Mose anali atagawira kale cholowa mafuko awiri ndi hafu kutsidya lina la Yorodano.+ Koma Alevi sanawapatse cholowa pakati pawo.+ 4 Ana a Yosefe anakhala mafuko awiri,+ la Manase+ ndi la Efuraimu.+ Iwowa anapatsa Alevi mizinda+ yoti azikhalamo, malo odyetserako ziweto, ndi osungirako katundu wawo, koma sanawagawire cholowa cha malo.+ 5 Ana a Isiraeli anagawadi dzikolo monga mmene Yehova analamulira Mose.
6 Tsopano ana a Yuda anapita kwa Yoswa ku Giligala.+ Ndipo Kalebe+ mwana wa Yefune Mkenizi,+ anauza Yoswa kuti: “Inu mukudziwa bwino za mawu amene Yehova analankhula+ kwa Mose munthu wa Mulungu woona,+ onena za ine ndi inu ku Kadesi-barinea.+ 7 Ndinali ndi zaka 40 pamene Mose mtumiki wa Yehova anandituma kukazonda dziko,+ kuchokera ku Kadesi-barinea. Nditabwerako ndinamuuza kuchokera pansi pa mtima wanga, zonse zimene ndinaona.+ 8 Anthu amene ndinapita nawo, anapangitsa mitima ya anthu kuchita mantha kwambiri.+ Koma ine ndinatsatira Yehova Mulungu wanga ndi mtima wonse.+ 9 Chotero Mose anandilumbirira tsiku limenelo kuti, ‘Dziko limene wakaliponda ndi mapazi ako+ lidzakhala cholowa chako ndi cha ana ako mpaka kalekale, chifukwa watsatira Yehova Mulungu wanga ndi mtima wako wonse.’+ 10 Yehova wandisunga ndi moyo+ monga mmene analonjezera.+ Tsopano padutsa zaka 45 kuchokera pamene Yehova analonjeza Mose, pa nthawi imene Aisiraeli anali m’chipululu,+ ndipo lero ndili ndi zaka 85. 11 Komabe ndikadali ndi mphamvu monga ndinalili pa tsiku limene Mose anandituma.+ Mmene mphamvu zanga zinalili pa nthawiyo, ndi mmenenso zilili panopa, moti ndikhoza kupita kunkhondo ndi kubwerako.+ 12 Choncho, ndipatseni dera lamapiri ili limene Yehova anandilonjeza pa tsiku lija.+ Pa tsikulo, ngakhale inuyo munamva kuti kumeneko kuli Aanaki+ ndi mizinda ikuluikulu yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.+ Koma mosakayikira Yehova akakhala nane,+ ndipo ndikawapitikitsa ndithu monga mmene Yehova analonjezera.”+
13 Pamenepo Yoswa anadalitsa Kalebe mwana wa Yefune, ndi kum’patsa mzinda wa Heburoni monga cholowa chake.+ 14 N’chifukwa chake mzinda wa Heburoni uli cholowa cha Kalebe mwana wa Yefune Mkenizi, kufikira lero. Anam’patsa mzindawo chifukwa iye anatsatira Yehova Mulungu wa Isiraeli ndi mtima wake wonse.+ 15 Zimenezi zisanachitike, mzinda wa Heburoni unkatchedwa Kiriyati-ariba+ (Ariba+ anali munthu wamphamvu pakati pa Aanaki). Ndipo dziko lonse linakhala bata, lopanda nkhondo.+