22 Pamene anali kusangalatsa mitima yawo,+ mwadzidzidzi amuna a mumzindawo, anthu opanda pake,+ anazungulira nyumbayo,+ ndipo anali kukankhanakankhana pachitseko. Iwo anali kuuza mwamuna wokalamba uja, mwini nyumbayo, kuti: “Tulutsa mwamuna amene wabwera m’nyumba yako kuti tigone naye.”+