7 Tembenukani ndi kulowera kudera lamapiri la Aamori+ ndi anthu oyandikana nawo onse okhala ku Araba,+ kudera lamapiri,+ ku Sefela, ku Negebu,+ m’mbali mwa nyanja,+ m’dziko la Akanani+ ndi ku Lebanoni+ mpaka kumtsinje waukulu wa Firate.+
6 Ine ndidzapitikitsa pamaso pa ana a Isiraeli anthu onse okhala kudera lamapiri, kuchokera ku Lebanoni+ mpaka ku Misirepotu-maimu,+ ndidzapitikitsa Asidoni onse.+ Iweyo ungopereka dzikoli kwa ana a Isiraeli+ kuti likhale cholowa chawo monga mmene ndinakulamulira.+