35 Iye anatumiza mithenga+ m’dera lonse la fuko la Manase, ndipo anthu a m’fuko limeneli nawonso anasonkhana pamodzi n’kuyamba kumutsatira. Anatumizanso mithenga m’madera onse a mafuko a Aseri, Zebuloni ndi Nafitali, ndipo nawonso anabwera kudzakumana naye.