50 Ukamakazunza ana angawa,+ ndipo ukakatenga akazi ena kuwonjezera pa ana anga, ngakhale palibe munthu pano, dziwa kuti Mulungu ndiye mboni pakati pa ine ndi iwe.”+
5 Atatero, iye anawayankha kuti: “Yehova ndi mboni yokutsutsani, ndipo wodzozedwa+ wake ndi mboni lero kuti simunandipeze ndi mlandu uliwonse.”+ Pamenepo iwo anati: “Inde, iyedi ndi mboni.”