28 Kenako Abisalomu analamula omutumikira kuti: “Muonetsetse chonde kuti Aminoni akangosangalala mumtima mwake ndi vinyo,+ ine n’kukuuzani kuti, ‘Mukantheni Aminoni!’ pamenepo mumuphe. Musaope.+ Kodi si ndine amene ndakulamulani? Chitani zinthu mwamphamvu ndipo khalani olimba mtima.”