Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Rute 3:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Boazi anadya ndi kumwa, ndipo anali wosangalala mumtima mwake.+ Kenako anapita kukagona chakumapeto kwa mulu wa balere. Ndiyeno Rute anayenda mwakachetechete ndi kuvundukula kumapazi kwa Boazi n’kugona.

  • 1 Samueli 25:36
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 36 Kenako Abigayeli anapita kwa Nabala ndipo anapeza kuti akuchita phwando m’nyumba mwake ngati phwando la mfumu.+ Nabala anali kusangalala kwambiri mumtima mwake ndipo anali ataledzereratu.+ Abigayeli sanamuuze chilichonse, chaching’ono kapena chachikulu, kufikira m’mawa mwake.

  • Esitere 1:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Pa tsiku la 7, pamene mtima wa mfumu unali kukondwera ndi vinyo,+ mfumu inauza Mehumani, Bizita, Haribona,+ Bigita, Abagata, Zetara ndi Karikasi, nduna 7 za panyumba ya mfumu zimene zinali kutumikira+ Mfumu Ahasiwero,

  • Salimo 104:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Komanso kuti mutuluke vinyo amene amasangalatsa mtima wa munthu.+

      Amachita zonsezi kuti nkhope ya munthu isalale ndi mafuta,+

      Komanso kuti apereke chakudya chimene chimakhutiritsa mtima wa munthu.+

  • Mlaliki 2:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Ndinafufuza ndi mtima wanga wonse kuti ndidziwe uchitsiru posangalatsa thupi langa ndi vinyo,+ pamene ndinali kutsogolera mtima wanga ndi nzeru.+ Ndinachita zimenezi kuti ndione ubwino umene ana a anthu amapeza pa zimene amachita padziko lapansi pano masiku onse a moyo wawo.+

  • Mlaliki 10:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Chakudya chimachititsa antchito kuseka, ndipo vinyo amachititsa moyo kusangalala,+ koma ndalama zimathandiza pa zinthu zonse.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena