Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Oweruza 9:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Poyankha mtengo wa mpesawo unati, ‘Kodi ndisiye vinyo wanga watsopano amene amasangalatsa Mulungu ndi anthu,+ n’kupita kuti ndizikagwedezeka pamwamba pa mitengo ina?’

  • 2 Samueli 13:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Kenako Abisalomu analamula omutumikira kuti: “Muonetsetse chonde kuti Aminoni akangosangalala mumtima mwake ndi vinyo,+ ine n’kukuuzani kuti, ‘Mukantheni Aminoni!’ pamenepo mumuphe. Musaope.+ Kodi si ndine amene ndakulamulani? Chitani zinthu mwamphamvu ndipo khalani olimba mtima.”

  • Esitere 1:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Pa tsiku la 7, pamene mtima wa mfumu unali kukondwera ndi vinyo,+ mfumu inauza Mehumani, Bizita, Haribona,+ Bigita, Abagata, Zetara ndi Karikasi, nduna 7 za panyumba ya mfumu zimene zinali kutumikira+ Mfumu Ahasiwero,

  • Miyambo 31:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Anthu inu, perekani chakumwa choledzeretsa kwa munthu amene watsala pang’ono kuwonongedwa+ ndi vinyo kwa anthu amene mtima wawo ukuwawa.+

  • Mlaliki 2:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Ndinafufuza ndi mtima wanga wonse kuti ndidziwe uchitsiru posangalatsa thupi langa ndi vinyo,+ pamene ndinali kutsogolera mtima wanga ndi nzeru.+ Ndinachita zimenezi kuti ndione ubwino umene ana a anthu amapeza pa zimene amachita padziko lapansi pano masiku onse a moyo wawo.+

  • Mlaliki 9:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Pita ukadye chakudya chako mokondwera ndi kumwa vinyo wako ndi mtima wosangalala,+ chifukwa Mulungu woona wakondwera kale ndi ntchito zako.+

  • Mlaliki 10:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Chakudya chimachititsa antchito kuseka, ndipo vinyo amachititsa moyo kusangalala,+ koma ndalama zimathandiza pa zinthu zonse.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena