Deuteronomo 16:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Uzichitira Yehova Mulungu wako chikondwerero chimenecho masiku 7+ pamalo amene Yehova adzasankhe. Uzichita chikondwerero chimenecho chifukwa Yehova Mulungu wako adzakudalitsa+ pa zokolola zako zonse ndi pa chilichonse chimene dzanja lako likuchita, ndipo iwe uzikhala wosangalala basi.+ Machitidwe 10:31 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 31 Munthuyo anandiuza kuti, ‘Koneliyo, Mulungu wamva pemphero lako, ndipo wakumbukira mphatso zako zachifundo.+ Machitidwe 10:35 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 35 Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.+ Machitidwe 14:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Komabe iye sanangokhala wopanda umboni wakuti anachita zabwino.+ Anakupatsani mvula+ kuchokera kumwamba ndi nyengo zimene zokolola zanu zimakhala zambiri. Anadzaza mitima yanu ndi chakudya komanso chimwemwe.”+
15 Uzichitira Yehova Mulungu wako chikondwerero chimenecho masiku 7+ pamalo amene Yehova adzasankhe. Uzichita chikondwerero chimenecho chifukwa Yehova Mulungu wako adzakudalitsa+ pa zokolola zako zonse ndi pa chilichonse chimene dzanja lako likuchita, ndipo iwe uzikhala wosangalala basi.+
31 Munthuyo anandiuza kuti, ‘Koneliyo, Mulungu wamva pemphero lako, ndipo wakumbukira mphatso zako zachifundo.+
17 Komabe iye sanangokhala wopanda umboni wakuti anachita zabwino.+ Anakupatsani mvula+ kuchokera kumwamba ndi nyengo zimene zokolola zanu zimakhala zambiri. Anadzaza mitima yanu ndi chakudya komanso chimwemwe.”+