16 Ndiyeno Rute anati: “Musandichonderere kuti ndikusiyeni, kuti ndibwerere ndisakutsatireni, pakuti kumene inu mupite inenso ndipita komweko, kumene inu mugone inenso ndigona komweko.+ Anthu a mtundu wanu adzakhala anthu a mtundu wanga,+ ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga.+