30 Ndiyeno uike Urimu+ ndi Tumimu m’chovala pachifuwa chachiweruzo, ndipo zizikhala pamtima pa Aroni akamalowa kukaonekera pamaso pa Yehova. Aroni azinyamula ziweruzo+ za ana a Isiraeli pamtima pake poonekera kwa Yehova nthawi zonse.
3 (Ahiya ndiye anali kunyamula efodi.+ Iye anali mwana wa Ahitubu,+ m’bale wa Ikabodi,+ mwana wa Pinihasi,+ mwana wa Eli,+ wansembe wa Yehova ku Silo.)+ Koma anthu sanadziwe kuti Yonatani wachoka.