2 Choncho anthu anapita kukamuuza Yehosafati kuti: “Kwabwera khamu lalikulu la anthu ochokera kuchigawo cha kunyanja,* ku Edomu,+ kudzamenyana nanu. Panopa iwo ali ku Hazazoni-tamara, kapena kuti ku Eni-gedi.”+
10 “Asodzi adzaimirira m’mbali mwa nyanjayo kuchokera ku Eni-gedi+ mpaka ku Eni-egilaimu. Kumeneko kudzakhala malo oyanikapo makoka. Nsombazo zidzakhala zambirimbiri, zamitundu yosiyanasiyana ngati nsomba za ku Nyanja Yaikulu.+