4 Taonani, ndinakupatsani malo a mitundu yonse imene yatsalayi mwa kuchita maere.+ Ndinakupatsaninso malo a mitundu imene ndinaiwononga+ kuchokera kumtsinje wa Yorodano, mpaka kolowera dzuwa, ku Nyanja Yaikulu, monga cholowa cha mafuko anu.+
28 Malire a kum’mwera a dzikolo akhale malire a gawo la fuko la Gadi a mbali ya kum’mwera. Malirewo achokere ku Tamara+ kukafika kumadzi a Meribati-kadesi,+ kuchigwa+ cha Iguputo, mpaka ku Nyanja Yaikulu.+