Miyambo 12:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Munthu amene amasonyeza mkwiyo wake tsiku lomwelo ndi wopusa,+ koma wochenjera akachitiridwa chipongwe, amangozinyalanyaza.+ Miyambo 14:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Munthu amene amakwiya msanga amachita zinthu zopusa,+ koma munthu wotha kuganiza bwino amadedwa.+ Miyambo 26:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Usayankhe aliyense wopusa mogwirizana ndi uchitsiru wake, kuti iweyo usafanane naye.+ Aroma 12:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Musalole kuti choipa chikugonjetseni, koma pitirizani kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino.+
16 Munthu amene amasonyeza mkwiyo wake tsiku lomwelo ndi wopusa,+ koma wochenjera akachitiridwa chipongwe, amangozinyalanyaza.+