21 Patapita nthawi, Davide anafika kwa amuna 200+ amene anawasiya kuchigwa cha Besori, amene sanathe kupita ndi Davide pakuti anali otopa kwambiri. Pamenepo iwo ananyamuka kudzakumana ndi Davide ndi anthu amene anali naye. Davide atawayandikira, anawafunsa za moyo wawo.