9 Kenako zimene zinachitika n’zakuti, atazungulira ndi likasalo n’kufika nalo kumeneko, dzanja la Yehova+ linasautsanso mzindawo ndi chisokonezo chachikulu kwambiri. Iye anayamba kukantha anthu onse a mumzindawo, osasiyapo aliyense moti onsewo anagwidwa ndi matenda a mudzi.+