1Tsopano panali mwamuna wina wa ku Ramatayimu-zofimu,+ kudera lamapiri la Efuraimu,+ dzina lake Elikana.+ Iye anali mwana wa Yerohamu, mwana wa Elihu, mwana wa Tohu, mwana wa Zufi+ Mwefuraimu.*
18 Choncho Davide anathawa ndi kupulumuka,+ moti anafika kwa Samueli ku Rama.+ Atafika kumeneko anasimbira Samueli zonse zimene Sauli anam’chitira. Kenako Davide ndi Samueli anachoka ndi kupita kukakhala ku Nayoti.+