8 Iye amadzutsa wonyozeka, kumuchotsa pafumbi.+
Amachotsa osauka padzala,+
Kuti awakhazike pakati pa anthu olemekezeka,+ ndipo amawapatsa mpando wachifumu waulemerero.+
Pakuti michirikizo ya dziko lapansi ndi ya Yehova,+
Ndipo anakhazika dziko lapansi pamichirikizo imeneyo.