Oweruza 9:54 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 54 Msangamsanga Abimeleki anaitana mtumiki wake womunyamulira zida ndi kumuuza kuti: “Tenga lupanga lako undiphe,+ kuopera kuti anthu anganene za ine kuti, ‘Anaphedwa ndi mkazi.’” Nthawi yomweyo, mtumiki wakeyo anamubaya* ndi lupanga, ndipo anafa.+ 1 Samueli 14:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Ndiyeno Yonatani anapita chokwawa,+ mtumiki wake akum’tsatira pambuyo. Pamenepo Yonatani+ anayamba kukantha Afilisitiwo ndipo mtumiki wake uja anali kumalizitsa kupha anthuwo m’mbuyo mwake.+ 1 Samueli 31:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Kenako Sauli anauza womunyamulira zida kuti: “Solola lupanga lako+ undibaye* nalo, kuti amuna osadulidwawa+ asandipeze ndi kundibaya komanso kundizunza.” Koma womunyamulira zida uja sanafune,+ chifukwa anali kuopa kwambiri. Chotero Sauli anatenga lupanga lake ndi kuligwera.+
54 Msangamsanga Abimeleki anaitana mtumiki wake womunyamulira zida ndi kumuuza kuti: “Tenga lupanga lako undiphe,+ kuopera kuti anthu anganene za ine kuti, ‘Anaphedwa ndi mkazi.’” Nthawi yomweyo, mtumiki wakeyo anamubaya* ndi lupanga, ndipo anafa.+
13 Ndiyeno Yonatani anapita chokwawa,+ mtumiki wake akum’tsatira pambuyo. Pamenepo Yonatani+ anayamba kukantha Afilisitiwo ndipo mtumiki wake uja anali kumalizitsa kupha anthuwo m’mbuyo mwake.+
4 Kenako Sauli anauza womunyamulira zida kuti: “Solola lupanga lako+ undibaye* nalo, kuti amuna osadulidwawa+ asandipeze ndi kundibaya komanso kundizunza.” Koma womunyamulira zida uja sanafune,+ chifukwa anali kuopa kwambiri. Chotero Sauli anatenga lupanga lake ndi kuligwera.+