7 Anamuuza mawu amenewa pamene magulu ankhondo a mfumu ya Babulo anali kumenyana ndi Yerusalemu ndi mizinda ina yonse ya mu Yuda,+ kuphatikizapo Lakisi+ ndi Azeka.+ Mizinda imeneyi inali ndi mipanda yolimba kwambiri+ ndipo ndi imene inali isanawonongedwe pamizinda ya mu Yuda.+