5 Pambuyo pake, Davide ananyamuka ndi kupita kumene Sauli anamanga msasa. Atafika kumeneko, Davide anaona pamene Sauli komanso Abineri+ mwana wa Nera, mtsogoleri wa gulu lankhondo, anagona. Sauli anali atagona mkati mwa mpanda wa msasa,+ ndipo anthu ena onse anagona momuzungulira.