50 Mkazi wa Sauli dzina lake anali Ahinowamu, mwana wamkazi wa Ahimazi. Mkulu wa gulu lake lankhondo anali Abineri+ mwana wa Nera, m’bale wa bambo ake a Sauli.
27 Abineri atabwerera ku Heburoni,+ Yowabu anam’tengera pambali kuchipata kuti alankhulane naye pa awiri.+ Koma kumeneko anamubaya pamimba+ moti anafa chifukwa chokhetsa magazi a Asaheli,+ m’bale wake wa Yowabu.