Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Samueli 14:50
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 50 Mkazi wa Sauli dzina lake anali Ahinowamu, mwana wamkazi wa Ahimazi. Mkulu wa gulu lake lankhondo anali Abineri+ mwana wa Nera, m’bale wa bambo ake a Sauli.

  • 1 Samueli 17:55
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 55 Sauli ataona Davide akupita kukakumana ndi Mfilisiti uja, anafunsa Abineri,+ mkulu wa asilikali, kuti: “Kodi ameneyu ndi mwana+ wa ndani,+ Abineri?” Poyankha Abineri anati: “Ndikulumbira pali moyo wanu mfumu, ine sindikudziwa ngakhale pang’ono!”

  • 1 Samueli 26:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Pambuyo pake, Davide ananyamuka ndi kupita kumene Sauli anamanga msasa. Atafika kumeneko, Davide anaona pamene Sauli komanso Abineri+ mwana wa Nera, mtsogoleri wa gulu lankhondo, anagona. Sauli anali atagona mkati mwa mpanda wa msasa,+ ndipo anthu ena onse anagona momuzungulira.

  • 2 Samueli 4:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Mwana+ wa Sauli atamva kuti Abineri wafa ku Heburoni,+ manja ake analefuka+ ndipo Aisiraeli onse anasokonezeka.

  • 1 Mafumu 2:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 “Iweyo ukudziwa bwino kwambiri zimene Yowabu mwana wa Zeruya anandichita,+ mwa kupha akulu awiri a asilikali a Isiraeli, Abineri+ mwana wa Nera ndi Amasa+ mwana wa Yeteri.+ Mwakutero, anakhetsa magazi+ ankhondo pa nthawi yamtendere. Ndipo anadetsa ndi magazi ankhondo lamba amene anali m’chiuno mwake ndiponso nsapato zimene zinali kuphazi kwake.

  • 1 Mbiri 26:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Panalinso zinthu zonse zimene Samueli wamasomphenya,+ Sauli mwana wa Kisi, Abineri+ mwana wa Nera, ndi Yowabu+ mwana wa Zeruya+ anaziyeretsa kukhala zopatulika. Chilichonse chimene munthu anachiyeretsa chinali kuyang’aniridwa ndi Selomiti ndi abale ake.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena