10 Koma Amasa sanachenjere ndi lupanga limene linali m’manja mwa Yowabu. Choncho Yowabuyo anamubaya+ nalo m’mimba ndipo matumbo ake anakhuthukira pansi, moti sanachite kumubaya kawiri. Chotero Amasa anafa. Pamenepo Yowabu ndi Abisai m’bale wake anathamangitsa Sheba mwana wa Bikiri.