25 Ndiyeno Abisalomu anasankha Amasa+ kukhala mtsogoleri wagulu lankhondo kulowa m’malo mwa Yowabu.+ Amasa anali mwana wa munthu wina dzina lake Itara,+ Mwisiraeli amene anagona ndi Abigayeli,+ mwana wamkazi wa Nahasi, mlongo wake wa Zeruya, mayi wake wa Yowabu.