3 Koma anthuwo anati: “Iyayi musapite,+ pakuti ngati titathawa kumeneko, sakasamala za ife.+ Ndipo ngati hafu ya ife tingafe, sakasamala za ife chifukwa inuyo ndinu wofunika kuposa anthu 10,000.+ Tsopano zingakhale bwino kuti muzititumikira ndi kutithandiza+ muli mumzinda mom’muno.”