8 Chotero mfumu inatenga Arimoni ndi Mefiboseti, amene anali ana awiri aamuna a Rizipa,+ mwana wamkazi wa Aya, amene Rizipayo anaberekera Sauli. Anatenganso ana aamuna asanu a Mikala,+ mwana wamkazi wa Sauli, amene anaberekera Adiriyeli,+ mwana wa Barizilai Mmeholati.