16 “‘Ngati wapereka mbali ina ya munda wake+ kwa Yehova kuti ikhale yopatulika, mtengo wa malowo uzikhala wogwirizana ndi mbewu zimene angabzalepo. Ngati angabzalepo balere wokwanira muyezo umodzi wa homeri,+ ndiye kuti mtengo wa malowo ndi masekeli asiliva 50.