27 Pamenepo mfumu inapitiriza kuuza Zadoki wansembe kuti: “Iwe ndi wamasomphenya,*+ si choncho kodi? Bwerera kumzinda mu mtendere. Bwerera pamodzi ndi Ahimazi mwana wako wamwamuna ndi Yonatani+ mwana wamwamuna wa Abiyatara. Mubwerere ndi ana anu awiri amene muli nawowa.
3 Davide ndi Zadoki,+ yemwe anali wochokera mwa ana a Eleazara, ndiponso Ahimeleki,+ wochokera mwa ana a Itamara, anagawa ana a Aroniwo m’magulu a udindo pa utumiki wawo.+