3 Mwana wake wachiwiri anali Kileyabu+ wobadwa kwa Abigayeli+ wa ku Karimeli, amene anali mkazi wa Nabala, ndipo wachitatu anali Abisalomu+ wobadwa kwa Maaka, mwana wamkazi wa Talimai+ mfumu ya ku Gesuri.
13Pambuyo pa zinthu zimenezi, zinachitika kuti, Abisalomu+ mwana wa Davide, anali ndi mlongo wake wokongola dzina lake Tamara.+ Ndipo Aminoni+ mwana wa Davide anayamba kukonda kwambiri+ Tamara.