14 Kenako Abisalomu ndi amuna onse a Isiraeli anati: “Malangizo a Husai Mwareki ndi abwino+ kusiyana ndi malangizo a Ahitofeli!” Ndipo Yehova anaonetsetsa+ kuti anthuwo asatsatire malangizo+ a Ahitofeli ngakhale kuti anali abwino.+ Yehova anachita zimenezi kuti adzetsere Abisalomu tsoka.+