13 Ndithudi, n’chifukwa chake ifenso timayamikadi+ Mulungu mosalekeza. Pakuti pamene munalandira mawu a Mulungu+ amene munamva kwa ife, simunawalandire monga mawu a anthu+ ayi, koma mmene alilidi, monga mawu a Mulungu. Mawu amenewa akugwiranso ntchito mwa inu okhulupirira.+