8 Ndiye inu lembani makalata m’malo mwa Ayuda. Mulembe zimene mukuona kuti n’zabwino kwa inu m’dzina la mfumu.+ Mudinde makalatawo ndi mphete yodindira ya mfumu, pakuti n’zosatheka kufafaniza makalata amene alembedwa m’dzina la mfumu ndi kudindidwa ndi mphete yake yodindira.”+