43 Mizinda yake ndi Bezeri,+ m’chipululu cha dera lokwererapo, wothawirako Arubeni, mzinda wa Ramoti+ ku Giliyadi, wothawirako Agadi, ndi mzinda wa Golani+ ku Basana, wothawirako Amanase.+
8 Kuchigawo chakum’mawa kwa Yorodano, m’dera la kufupi ndi Yeriko, kunali Bezeri+ m’chipululu cha m’dera lokwererapo la fuko la Rubeni.+ Kunalinso Ramoti+ ku Giliyadi m’dera la fuko la Gadi, ndi Golani+ ku Basana m’dera la fuko la Manase.
13 mwana wa Geberi ku Ramoti-giliyadi+ (dera lake linali midzi ing’onoing’ono ya Yairi+ mwana wa Manase, yomwe ili ku Giliyadi.+ Analinso ndi chigawo cha Arigobi,+ chomwe chili ku Basana.+ Kunali mizinda ikuluikulu 60 yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri ndiponso mipiringidzo yamkuwa),