5 Davide pamodzi ndi nyumba yonse ya Isiraeli anali kusangalala pamaso pa Yehova, akuimba mitundu yonse ya zoimbira za mtengo wofanana ndi mtengo wa mkungudza. Anali kuimbanso zeze,+ zoimbira za zingwe,+ zinganga+ ndi maseche+ osiyanasiyana.
15 Makoma a mkati mwa nyumbayo anawamanga ndi matabwa akuluakulu a mkungudza. Mkati mwa nyumbayo, kuchokera pansi mpaka kudenga* anakutamo ndi matabwa. Kenako anakuta pansi pa nyumbayo ndi matabwa akuluakulu a mitengo yofanana ndi mkungudza.+