6 Iye anapanganso mabeseni 10. Anaika mabeseni asanu mbali ya kudzanja lamanja, mabeseni asanu mbali ya kumanzere.+ M’mabeseniwo anali kutsukiramo ndi kutsukuluziramo+ zinthu zokhudzana ndi nsembe yopsereza.+ Ansembe anali kusamba madzi ochokera m’thanki ija.+