9 Kenako mfumukaziyo inapatsa mfumuyo golide wokwana matalente 120,+ mafuta a basamu+ ochuluka zedi, ndi miyala yamtengo wapatali.+ Mafuta a basamu amene mfumukazi ya ku Sheba inapatsa Mfumu Solomo, anali ochuluka kwambiri moti sipanakhalenso mafuta ochuluka ngati amenewo.+