7 Kodi ndani amene sangakuopeni,+ inu Mfumu ya mitundu yonse?+ Inuyo ndinu woyenera kuopedwa, chifukwa chakuti pakati pa anzeru onse a m’mitundu ya anthu ndiponso pakati pa maufumu awo onse, palibiretu aliyense wofanana ndi inu.+
26 Ine ndikulamula+ kuti m’zigawo zonse za ufumu wanga, anthu azinjenjemera ndi kuchita mantha pamaso pa Mulungu wa Danieli.+ Pakuti iye ndi Mulungu wamoyo, amene adzakhalapo mpaka kalekale+ ndipo ufumu wake+ sudzawonongeka+ komanso ulamuliro wake udzakhalapo kwamuyaya.+