Miyambo
8 Nzerutu ikungokhalira kufuula,+ ndipo kuzindikira kukungokhalira kutulutsa mawu.+ 2 Imaima pamwamba pa zitunda,+ m’mbali mwa njira ndi pamphambano za misewu. 3 Imafuula mokweza+ pambali pa zipata, pakhomo la mzinda ndi polowera kuzipata,+ kuti:
4 “Ndikufuulira anthu inu, ndipo mawu anga akupita kwa ana a anthu.+ 5 Inu osadziwa zinthu, phunzirani kukhala ochenjera.+ Anthu opusa inu, pezani mtima womvetsa zinthu.+ 6 Mvetserani chifukwa ndikulankhula zinthu zofunika kwambiri.+ Ndikutsegula pakamwa panga kuti ndinene zowongoka.+ 7 Pakuti pakamwa panga pamalankhula choonadi motsitsa,+ ndipo milomo yanga imaipidwa ndi zoipa.+ 8 Mawu onse otuluka pakamwa panga ndi olungama.+ Pa mawu anga palibe zokhota kapena zopotoka.+ 9 Mawu anga onse ndi osavuta kumva kwa wozindikira, ndipo ndi owongoka kwa anthu odziwa zinthu.+ 10 Landirani malangizo* anga osati siliva, ndiponso kudziwa zinthu m’malo mwa golide wabwino kwambiri.+ 11 Pakuti nzeru n’zamtengo wapatali kuposa miyala ya korali,+ ndipo zosangalatsa zonse sizingafanane nazo.+
12 “Ine nzeru, ndimakhala pamodzi ndi kuchenjera,+ ndimadziwa zinthu, ndiponso ndimatha kuganiza bwino.+ 13 Kuopa Yehova kumatanthauza kudana ndi zoipa.+ Ndimadana ndi kudzikweza, kunyada,+ njira yoipa ndiponso pakamwa ponena zopotoka.+ 14 Ine ndili ndi malangizo+ ndi nzeru zopindulitsa.+ Ndimamvetsa zinthu,+ ndiponso ndili ndi mphamvu.+ 15 Chifukwa cha ine, mafumu amalamulira. Nazonso nduna zapamwamba zimakhazikitsa malamulo olungama.+ 16 Chifukwa cha ine, akalonga amalamulira,+ ndipo anthu onse olemekezeka amaweruza mwachilungamo.+ 17 Amene amandikonda, inenso ndimawakonda.+ Amene amandifunafuna ndi amene amandipeza.+ 18 Chuma ndi ulemerero zili ndi ine.+ Ndilinso ndi cholowa chamtengo wapatali ndi chilungamo.+ 19 Zipatso zanga n’zabwino kuposa golide. N’zoposa ngakhale golide woyengedwa bwino. Zokolola zanga n’zoposa siliva wabwino kwambiri.+ 20 Ndimayenda m’njira yachilungamo,+ komanso pakati pamisewu yachilungamo,+ 21 kuti ndichititse amene amandikonda kulandira zinthu zamtengo wapatali,+ ndipo ndimadzazitsa nkhokwe zawo.+
22 “Yehova anandipanga monga chiyambi cha njira yake.+ Ine ndiye ntchito yoyambirira pa ntchito zake zimene anakwaniritsa kalekale kwambiri.+ 23 Ndinakhazikitsidwa kuyambira nthawi yosadziwika,+ kuyambira pa chiyambi, kuyambira nthawi zakale kuposa dziko lapansi.+ 24 Ndinabadwa ndi ululu wa pobereka kulibe madzi akuya,+ kulibe akasupe odzaza madzi. 25 Mapiri akuluakulu asanakhazikitsidwe,+ mapiri ang’onoang’ono asanakhalepo, ine ndinabadwa ndi ululu wa pobereka, 26 iye asanapange dziko lapansi,+ zigwa zopanda kanthu, ndi zibuma zoyamba za dothi lachonde la padziko lapansi.+ 27 Pamene anali kukonza kumwamba, ine ndinali pomwepo.+ Pamene anakhazikitsa lamulo lakuti pamwamba pa madzi akuya pazioneka pozungulira,+ 28 pamene analimbitsa mitambo yakumwamba,+ pamene anachititsa kuti akasupe a madzi akuya akhale olimba,+ 29 pamene anaikira nyanja lamulo lake lakuti madzi ake asapitirire pamene anawalamula,+ pamene anakhazikitsa maziko a dziko lapansi,+ 30 ine ndinali pambali pake monga mmisiri waluso.+ Tsiku ndi tsiku, iye anali kusangalala kwambiri ndi ine.+ Ineyo ndinkakhala wosangalala pamaso pake nthawi zonse.+ 31 Ndinali kusangalala ndi nthaka ya dziko lake lapansi,+ ndipo zinthu zimene zinali kundisangalatsa, zinali zokhudzana ndi ana a anthu.+
32 “Tsopano ananu, ndimvereni. Ndithu, odala ndiwo amene amasunga njira zanga.+ 33 Mverani malangizo kuti mukhale anzeru,+ ndipo musawanyalanyaze.+ 34 Wodala ndi munthu amene amandimvetsera mwa kukhala maso pamakomo anga tsiku ndi tsiku, mwa kuyang’anitsitsa pamafelemu a makomo anga.+ 35 Pakuti wondipeza ine, ndithu adzapezanso moyo+ ndipo Yehova adzasangalala naye,+ 36 koma wolephera kundipeza akupweteka moyo wake.+ Onse odana ndi ine ndiye kuti amakonda imfa.”+