9 Ana a Isiraeli anayamba kuchita zinthu zosayenera kwa Yehova Mulungu wawo,+ ndipo anapitiriza kumanga malo okwezeka+ m’mizinda yawo yonse, kuyambira kunsanja+ ya alonda mpaka kumzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri.
10 Iye anamanganso nsanja+ m’chipululu ndipo anakumba zitsime zambiri (popeza anakhala ndi ziweto zambiri). Anapanganso zomwezo ku Sefela+ ndi kudera lokwererapo. Kumapiri ndi ku Karimeli kunali alimi ndi anthu osamalira minda ya mpesa popeza iye ankakonda ulimi.