7 “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Anthu inu mukauze mfumu ya Yuda imene yakutumani kuno kudzafunsira uthenga wa Mulungu kwa ine+ kuti: “Taonani! Gulu lankhondo la Farao limene likubwera kwa anthu inu kuti likuthandizeni lidzabwerera kwawo ku Iguputo.+